Exodus 32:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ine ndidaŵauza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi golide abwere naye.’ Ndipo amene anali nazo zinthu zopangidwa ndi golide adandipatsa. Ndidaziponya pa moto, ndipo ndidapanga fano la mwanawang'ombe lija.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinanena nao, Aliyense ali naye golide amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinachiponya m'moto, ndimo anatulukamo mwanawang'ombe uyu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ine ndinawawuza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi zokometsera zagolide azivule.’ Choncho iwo anandipatsa golide, ndipo ndinamuponya pa moto ndi kupanga fano la mwana wangʼombeyu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinanena nao, Ali yense ali naye golidi amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinaciponya m'moto, ndimo anaturukamo mwana wa ng'ombe uyu.