Exodus 32:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo Mose adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Aliyense mwa inu atenge lupanga, ndipo mupite ku mahema ndi kuloŵa m'zipata zonse. Aliyense mwa inu akaphe mbale wake kapena bwenzi lake kapena mnansi.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Yense amange lupanga lake m'chuuno mwake, napite, nabwerere kuyambira chipata kufikira chipata, pakati pa chigono, naphe yense mbale wake, ndi yense bwenzi lake, ndi yense mnansi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena, ‘Pitani ku misasa konse, mulowe ku zipata zonse ndipo aliyense akaphe mʼbale wake, kapena mnzake kapena mnansi wake.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Yense amange lupanga lace m'cuuno mwace, napite, nabwerere kuyambira cipata kufikira cipata, pakati pa cigono, naphe yense mbale wace, ndi yense bwenzi lace, ndi yense mnansi wace.