Exodus 32:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake Mose adauza anthu kuti, “Inu mudachimwa koopsa. Koma tsopano ndidzapita kwa Chauta ku phiri, ndipo nditakupemphererani, kapena angathe kukukhululukirani machimo anu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose anati kwa anthu, Mwachimwa kuchimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzachita chotetezera uchimo wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake Mose anati kwa anthu onse, “Inu mwachita tchimo lalikulu. Koma tsopano ine ndipita ku phiri kwa Yehova mwina ndikatha kukupepeserani chifukwa cha tchimo lanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali m'mawa mwace, kuti Mose anati kwa anthu, Mwacimwa kucimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzacita cotetezera ucimo wanu.