Exodus 32:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano pita uŵatsogolere anthuwo ku malo amene ndidakuuza. Kumbukira kuti mngelo wanga adzakutsogolera, koma tsiku likubwera limene ndidzaŵalange iwowo chifukwa cha machimo ao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kunka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano pita ukawatsogolere anthu kumalo kumene ine ndinanena, ndipo mngelo wanga adzakutsogolerani. Komabe, nthawi yanga ikadzafika kuti ndiwalange, ndidzawalanga chifukwa cha tchimo lawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kumka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga cifukwa ca kucimwa kwao.