Exodus 32:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aroni adalandira golideyo kumanja kwa anthuwo, ndipo adamsungunula, napanga fano la mwanawang'ombe m'chikombole. Ndipo anthu adayamba kufuula kuti, “Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Aaroni analandira golideyo ndipo anamuwumba ndi chikombole ndi kupanga fano la mwana wangʼombe. Kenaka anthu aja anati, “Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anazilandira ku manja ao, nacikonza ndi cozokotera, naciyenga mwana wa ng'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto.