Exodus 32:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho m'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, adapereka nsembe zopsereza, nabweranso ndi nsembe zamtendere. Ndipo anthuwo adakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa, kenaka adayambanso kuvina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mawa mwake anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero tsiku linalo anthu anadzuka mmamawa ndithu ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Atatha kupereka nsembezo, anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mawa mwace anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.