Exodus 33:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Uchokeko kuno pamodzi ndi anthu amene udabwera nawo kuchokera ku Ejipito, ndipo upite ku dziko limene ndidalonjeza kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Pa nthaŵi imeneyo ndidaŵauza iwowo kuti, ‘Dziko limeneli ndidzalipatsa kwa zidzukulu zanu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m'dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anati, “Chokani pa malo ano, iwe ndi anthu amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto. Pitani ku dziko limene ine ndinalonjeza ndi lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo kuti, ‘Ine ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kucokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kucokera m'dziko la Aigupto, kumka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;