Exodus 33:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adauza Chauta kuti, “Mwakhala mukundiwuza kuti ndiŵatsogolere anthuŵa ku dzikolo, koma simudandiwuze amene mudzamtuma kuti apite nane. Komabe mwanena kale kuti, ‘Ndikukudziŵa bwino iwe, ndipo ndakondwa nawe.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitsa amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, ‘Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitsa amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga,