Exodus 33:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga zidzadziŵika bwanji kuti mwandikomera mtima ine pamodzi ndi anthu anu? Kodi si chifukwa chakuti mumapita nafe, ine pamodzi ndi anthu anu, kuti tizikhala osiyana ndi anthu ena onse a pa dziko lapansi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chidziwika ndi chiyani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi wina adzadziwa bwanji kuti inu mwandikomera mtima pamodzi ndi anthu awa ngati simupita nafe? Kodi nʼchiyani chomwe chidzatisiyanitse pakati pa anthu onse amene ali pa dziko lapansi?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti cidziwfka ndi ciani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi?