Exodus 33:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti Chauta anali atauza Mose kuti, “Uza Aisraelewo kuti, ‘Ndinu anthu okanika. Ndikadapita nanu pamodzi, ngakhale kamphindi kakang'ono kokha, bwenzi nditakuwonongani kwathunthu. Tsopano vulani zokongoletsa zanu, ndipo ndidzadziŵa choti ndingathe kukuchitani.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israele, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamodzi, ndidzakuthani; koma tsopano, vulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe chomwe ndikuchitireni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yehova anali atanena kwa Mose kuti, “Awuze Aisraeli kuti, ‘Inu ndinu nkhutukumve.’ Ngati ine ndipita ndi inu kwa kanthawi, nditha kukuwonongani. Tsopano vulani zodzikometsera zanu ndipo ine ndidzaganiza choti ndichite nanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israyeli, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamadzi, ndidzakuthani; koma tsopano, bvulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe comwe ndikucitireni.