Exodus 33:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose ankatenga chihema chija ndi kukachimanga kunja kwake kwa mahema, chapatali ndithu. Tsono adachitcha chihemacho dzina loti, “Chihema chamsonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Chauta ankatuluka kumahemako, napita ku chihema chamsonkhanocho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mose ankatenga tenti ndi kukayimanga kunja kwa msasa chapatalipo, ndipo ankayitcha “tenti ya msonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Yehova amapita ku tenti ya msonkhano kunja kwa msasa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose akatenga cihemaco nacimanga kunja kwa cigono, kutari kwa cigono; nacicha, Cihema cokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anaturuka kumka ku cihema cokomanako kunja kwa cigono.