Exodus 33:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi zonse Mose akamapita kuchihemako, anthu onse ankaimirira. Tsono aliyense ankangoimirira pakhomo pa hema lake, namayang'ana Moseyo mpaka ataloŵa m'chihema chokumaniranako ndi Chauta chija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakutuluka Mose kunka ku chihemacho kuti anthu onse anaimirira, nakhala chilili, munthu yense pakhomo pa hema wake, nachita chidwi pa Mose, kufikira atalowa m'chihemacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo nthawi ina iliyonse imene Mose amapita ku tenti anthu onse amanyamuka ndi kuyimirira pa makomo amatenti awo, kumuyangʼana Mose mpaka atalowa mu tentimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakuturuka Mose kumka ku cihemaco kuti anthu onse anaimirira, nakhala ciriri, munthu yense pakhomo pa hema wace, nacita cidwi pa Mose, kufikira atalowa m'cihemaco.