Exodus 34:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Chauta adati, “Ndidzachita nanu chipangano. Ndidzachita zozizwitsa zazikulu pamaso pa anthu ako onseŵa, zimene sizidachitikepo ndi kale lonse pa dziko lonse lapansi, pakati pa mitundu ina yonse. Anthu onse amene ali ndi iweŵa adzaona zimene Ine Chauta ndingathe kuchita, chifukwa zimene ndidzachita kudzera mwa iwe nzoopsa zedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anati, Taona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitika zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova anati: “Ine ndikuchita nanu pangano. Ndidzachita zodabwitsa pamaso pa anthu onse zimene sizinachitikenso ndi mtundu wina uliwonse wa anthu pa dziko lonse lapansi. Anthu amene mudzakhala pakati pawo adzaona kuopsa kwa ntchito imene Ine Yehova ndidzakuchitireni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati, Taona, Ine ndicita pangano; ndidzacita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinacitika zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uti wonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona nchito ya Yehova, pakuti cinthu ndikucitiraci ncoopsa.