Exodus 34:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku dziko limenelo, musadzachite nawo chipangano, chifukwa akamadziipitsa popembedza milungu yao nkumaiphera nsembe, kapena adzakuitanani kuti mudye nao chakudya cha nsembe zaozo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ungachite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa iwo akamakachita zadama ndi milungu yawo ndi kupereka nsembe, adzakuyitanani ndipo inu mudzadya nsembe zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ungacite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angacite cigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zace;