Exodus 34:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwina ana anu aamuna angathenso kumadzakwatira ana ao aakazi. Tsono akazi ameneŵa akamadziipitsa potumikira milungu yao, adzakopa ana anu aamuna kuti azidzatumikiranso milungu yaoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ungatengereko ana ako amuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao akazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo inu mukasankha ena mwa ana awo aakazi kukhala akazi a ana anu, akaziwo akakachita zadama ndi milungu yawo, akatsogolera ana anu aamuna kuchita chimodzimodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ungatengereko ana ako amuna ana ao akazi; nangacite cigololo ana ao akazi potsata milungu yao, ndi kucititsa ana anu amuna cigololo potsata milungu yao.