Exodus 34:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma muzidzaombola mwana woyamba kubadwa wa bulu, pakupereka nkhosa m'malo mwake. Mukapanda kumuwombola, muzidzamthyola khosi. Mwana aliyense wachisamba wamwamuna, muzidzachita choombola. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaonekere pamaso panga opanda kanthu kumanja kodzapereka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma woyamba wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu amuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muziwombola mwana woyamba kubadwa wa bulu popereka mwana wankhosa. Mukapanda kumuwombola mupheni. Muziwombola ana anu onse aamuna. “Palibe ndi mmodzi yemwe adzaonekere pamaso panga wopanda kanthu mʼdzanja lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma woyamba wa buru uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu amuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.