Exodus 34:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muzigwira ntchito pa masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, musagwire ntchito iliyonse, ngakhale pa nthaŵi yolima kapena yokolola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, koma lachisanu ndi chiwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri, musagwire ntchito ina iliyonse, Ngakhale nthawi yolima ndi yokolola muyenera kupuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku asanu ndi limodzi uzigwira nchito, koma lacisanu ndi ciwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula.