Exodus 34:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Musapereke buledi wofufumitsa pamene mukupereka kwa Ine magazi a nsembe yanga. Nyama iliyonse yophera nsembe ya Paska, musaisunge mpaka m'maŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi nsembe yophera ya chikondwerero cha Paska asaisiye kufikira m'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti, ndipo musasunge nsembe ya pa Chikondwerero cha Paska mpaka mmawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wacotupitsa; ndi nsembe yophera ya madyerero a Paskha asaisiye kufikira m'mawa.