Exodus 34:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzibwera ndi zokolola zoyamba ndi zabwino kwambiri ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu. Musaphike kamwanakanyama mu mkaka wa make.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako ku nyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwana wa mbuzi mu mkaka wa mace.