Exodus 34:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Mose adatsika phiri la Sinai atanyamula miyala iŵiri yaumboni ija, sadadziŵe kuti nkhope yake njoŵala chifukwa cholankhula ndi Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali pakutsika Mose pa phiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m'dzanja lake la Mose, pakutsika iye m'phirimo, Mose sanadziwe kuti khungu la nkhope yake linanyezimira popeza Iye adalankhula naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anatsika kuchokera mʼPhiri la Sinai pamodzi ndi miyala iwiri ija ya pangano mʼmanja mwake. Iye sanazindikire kuti nkhope yake imanyezimira pakuti anayankhula ndi Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali pakutsika Mose pa phiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m'dzanja lace la Mose, pakutsika iye m'phirimo, Mose sanadziwa kuti khungu la nkhope yace linanyezimira popeza iye adalankhula naye.