Exodus 34:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthuwo ankaona kuti nkhope yake njoŵala, koma Moseyo ankadziphimbanso kumaso mpaka nthaŵi ina yakuti apitenso kukalankhula ndi Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
iwo amaona nkhope yake ikunyezimira. Choncho Mose amaphimba nkhope yake ngakhale pamene amapita kukayankhula ndi Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso cophimba pankhope pace, kufikira akalowa kulankhula ndi iye.