Exodus 35:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri, lidzakhala la Sabata, tsiku lanu lopumula, loperekedwa kwa Chauta. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo, adzaphedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku la chisanu ndi chiwiri likhale la Sabata, tsiku lanu lopuma, lopatulika kwa Yehova. Aliyense amene adzagwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuphedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku asanu ndi limodzi azigwira nchito; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: ali yense agwira nchito pamenepo, aphedwe,