Exodus 35:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo munthu aliyense, monga momwe mtima wake unkafunira, adabwera kwa Chauta ndi zopereka zopangira chihema chamsonkhano cha Chauta. Adabwera nazo zonse zogwiritsira ntchito potumikira, ndi zonse zopangira zovala zopatulika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo aliyense amene anakhudzidwa mu mtima mwake nafuna kupereka, anabwera kudzapereka chopereka kwa Yehova cha ntchito yokonza tenti ya msonkhano, cha ntchito zonse za mʼtentimo ndi cha zovala zopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza, ali yense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wace wamfunitsa, nabwera naco copereka ca Yehova, ca ku nchito ya cihema cokomanako, ndi ku utumiki wace wonse, ndi ku zobvala zopatulika.