Exodus 35:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kudabwera amuna ndi akazi omwe. Munthu aliyense malinga ndi kufuna kwake adabwera ndi zokometsera zomangira zovala, nsapule zakukhutu, mphete, ukufu wam'khosi, ndi zokometsera zina zagolide. Munthu aliyense adabwera ndi zagolide zimene adazipatula kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zigwinjiri, zonsezi zokometsera za golide; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ace, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zidzingwiri, zonsezi zokometsera zagolidi; inde yense wakupereka kwa Yehova copereka cagolidi.