Exodus 35:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu aliyense amene anali ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, bafuta wa thonje losalala kwambiri, nsalu za ubweya wambuzi, zikopa zankhosa zonyika mu utoto wofiira, ndi zikopa zambuzi, adabwera nazo kwa Chauta. Aliyense adabwera ndi zimene anali nazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aliyense kwao kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene anali ndi nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo kapena yofiira kapena yofewa, yosalala, kapena ubweya wambuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira kapena zikopa anazibweretsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ali yense kwao kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.