Exodus 35:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse amene anali ndi siliva kapena mkuŵa, zonsezo adabwera nazo kwa Chauta. Onse amene anali ndi matabwa a mtengo wa kasiya wogwiritsira ntchito pomangapo, adabwera nawo ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yense wakupereka chopereka cha siliva ndi mkuwa, anabwera nacho chopereka cha Yehova; ndi yense amene kwao kunapezeka mtengo wakasiya wa ku machitidwe onse a ntchitoyi, anabwera nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene anapereka chopereka cha siliva kapena mkuwa anabweretsa monga chopereka kwa Yehova. Ndipo aliyense amene anali ndi matabwa a mtengo wa mkesha kuti awagwiritse ntchito mbali ina iliyonse ya ntchitoyo, anabweretsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yense wakupereka copereka ca siliva ndi mkuwa, anabwera naco copereka ca Yehova; ndi yense amene kwao kunapezeka mtengo wasitimu wa ku macitidwe onse a nchitoyi, anabwera nao.