Exodus 35:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Aisraele onse, amuna ndi akazi omwe, amene adafuna ndi mtima wao wonse kupereka zao ku ntchito zimene Chauta adalamula kudzera mwa Mose, adabwera ndi zopereka zao kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova anauza ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli onse aamuna ndi aakazi amene anali ndi mtima wofuna, anabweretsa kwa Yehova chopereka chaufulu ku ntchito yonse ya Yehova imene analamulira kudzera mwa Mose kuti achite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amuna ndi akazi onse a ana a Israyeli amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku nchito yonse imene Yehova anauza Ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera naco copereka cofuna mwini, kucipereka kwa Yehova.