Exodus 36:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndipo Bezalele, Oholiyabu, pamodzi ndi aluso onse amene Chauta adaŵapatsa luso ndi nzeru zodziŵira kupanga zofunika zonse zomangira malo opatulika, adzapanga zonse iwowo, monga momwe Chauta adalamulira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anachita Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m'mtima mwao adziwe machitidwe ake a ntchito yonse ya utumiki wake wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Bezaleli, Oholiabu pamodzi ndi anthu aluso onse amene Yehova anawapatsa luso ndi nzeru zodziwira kupanga zofunika zonse zomangira malo opatulika, adzapanga zonse iwowo, monga momwe Yehova analamulira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aholiabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m'mtima mwao adziwe macitidwe ace a nchito yonse ya utumiki wace wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova.