Exodus 36:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adasoka magonga a tinsalu tobiriŵira m'mphepete mwa chimodzi kubwalo kwake, ndipo adachitanso chimodzimodzi ndi chinacho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika magango ansalu yamadzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi ku mkawo wa chilumikizano; nachita momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano chachiwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anapanga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika magango ansaru yamadzi m'mphepete mwace mwa nsaru imodzi ku mkawo wa cilumikizano; nacita momwemo m'mphepete mwace mwa nsaru ya kuthungo, ya cilumikizano caciwiri.