Exodus 36:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adapanga chophimbira china chofiira cha zikopa za nkhosa zamphongo. Potsiriza adapanganso chophimbira china cha zikopa zofeŵa, nkuchiika pamwamba pa zophimba zina zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anapanga chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake anapanganso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anasokera hemalo cophimba ca zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi cophimba ca zikopa za akatumbu pamwamba pace.