Exodus 36:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Mose adaitana Bezalele, Oholiyabu ndi onse aluso amene Chauta adaŵapatsa nzeru, ndiponso onse amene anali okonzeka kuthandiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose adaitana Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m'mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kuntchito kuichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mose anayitana Bezaleli ndi Oholiabu ndiponso munthu aliyense waluso amene Yehova anamupatsa luso ndiponso amene anali ndi mtima wofuna kugwira ntchito.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose adaitana Bezaleli ndi Aholiabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m'mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kunchito kuicita.