Exodus 36:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndi masinde makumi anai chapansi pake. Pa fulemu lililonse adapanga masinde aŵiri asiliva, ogwirana ndi zolumikizira ziŵiri zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
napanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiponso anapanga matsinde 40 asiliva ndipo anawayika pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse anayika matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napanga makamwa makumi anai pansi pamatabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yace iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yace iwiri.