Exodus 36:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafulemu aŵiri am'ngodyawo anali olumikizika pansi pake ndi ogwirizana mpaka pamwamba ku ngoŵe yokoŵera yoyamba ija. Ndimo m'mene mafulemu aŵiri opanga ngodya ziŵiri aja adapangidwira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaphatikizika pamodzi patsinde, naphatikizika pamodzi pamutu pake ndi mphete imodzi; anatero nao onse awiri pangodya ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa ngodya ziwirizi panali maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba atalumikizidwa pa ngowe imodzi. Maferemu onse anali ofanana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaphatikizika pamodzi patsinde, naphatikizilca pamodzi pamutu pace ndi mphete imodzi; anatero nao onse awiri pa ngondya ziwiri.