Exodus 36:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Mose adaŵapatsa zopereka zonse zaufulu zomangira malo opatulika zimene Aisraele adabwera nazo. Koma Aisraelewo ankapatsabe Mose zopereka zao m'maŵa mulimonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analandira kwa Mose chopereka chonse, chimene ana a Israele adabwera nacho chikhale cha machitidwe a ntchito ya malo opatulika, aipange nacho. Koma anaonjeza kubwera nazo kwa iye zopereka zaufulu, m'mawa ndi m'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo analandira kuchokera kwa Mose zopereka zonse Aisraeli anabweretsa kuti agwirire ntchito yomanga malo wopatulika. Ndipo anthu anapitirira kupereka zopereka zaufulu mmawa uliwonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analandira kwa Mose copereka conse, cimene ana a Israyeli adabwera naco cikhale ca macitidwe a nchito ya malo opatulika, aipange naco. Koma anaonjeza kubwera nazo kwa iye zopereka zofuna mwini, m'mawa ndi m'mawa.