Exodus 36:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adapanga nsalu yochingira yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndipo adapetapo zithunzi za akerubi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaomba nsalu yotchinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anachiomba ndi akerubi ntchito ya mmisiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanga nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo inali yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso anapetapo zithunzi za Akerubi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaomba nsaru yocinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anaciomba ndi akerubi nchito ya mmisiri.