Exodus 36:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chipata choloŵera m'chihemamo, adaikapo nsalu yochinga yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso nsalu ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaomba nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanga nsalu ya pa chipata cholowera mu chihema, yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira yomwe inali yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaomba nsaru yotsekera pa khomo la cihemaco, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula;