Exodus 36:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adapanga nsanamira zisanu zokhala ndi ngoŵe zokoŵera nsaluyo, ndipo mitu yake ndi mitanda yake adaikuta ndi golide, koma masinde ake anali amkuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsanamira zake zisanu ndi zokowera zao; nakuta mitu yao ndi mitanda yao ndi golide; ndi makamwa ao asanu anali amkuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanga nsanamira zisanu ndi ngowe zake. Anakuta pamwamba pa nsanamirazo ndi zomangira zake ndi golide, ndipo anapanganso matsinde asanu amkuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsamamira zace zisanu ndi zokowera zao; nakuta mitu yao ndi mitanda yao ndi golidi; ndi makamwa ao asanu anali amkuwa.