Exodus 36:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
nadzauza Mose kuti, “Anthu akubwera ndi zipangizo za ntchitoyi zochuluka, kuposa m'mene zidzafunikire pogwira ntchito imene Chauta adalamula kuti ichitike.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zochuluka, zakuposera zoyenera ntchito imene Yehova anauza ichitike.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anati kwa Mose, “Anthu akubweretsa kuposa zimene zikufunika kugwirira ntchito imene Yehova analamulira kuti ichitike.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zocuruka, zakuposera zoyenera nchito imene Yehova anauza icitike.