Exodus 36:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Mose adalamula anthu m'mahema monse kuti, “Mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense asaperekenso zopereka zomangira malo opatulika.” Motero anthu adaleka kubwera ndi zopereka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mwa chigono chonse, ndi kuti, Asaonjezere ntchito ya ku chopereka cha malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Mose analamulira ndipo analengeza mu msasa onse, “Mwamuna kapena mayi aliyense asaperekenso chopereka chilichonse cha ku malo wopatulika.” Choncho anthu analetsedwa kubweretsa zambiri,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mwa cigono conse, ndi kuti, Asaonjezere nchito ya ku copereka ca malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina.