Exodus 36:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono amuna onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo, adapanga chihema cha Chauta ndi nsalu khumi za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndiponso ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira. Pa nsalu zonsezo adapetapo zithunzi za akerubi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga Kachisi ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi akerubi, ntchito ya mmisiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo anapanga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso anapeta pa nsaluzo Akerubi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akucita nchitoyi anapanga kacisi ndi nsaru zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi; ndi lofiira, ndi lofiira, ndi akerubi, nchito ya mmisiri.