Exodus 36:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'litali mwa nsalu iliyonse munali mamita 13, ndipo muufupi mwake munali masentimita 183. Zonsezo zinali zofanana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi mikono inai; nsalu zonse zinafanana muyeso wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nsalu zonse zinali zofanana. Mulitali mwake zinali mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Utali wace wa nsaru yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi mikono inai; nsaru zonse zinafanana muyeso wao.