Exodus 37:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapanganso ziŵiya za golide wabwino kwambiri za pa tebulolo, monga mbale, zikho, mitsuko ndi mabeseni ogwiritsira ntchito pa zopereka zamadzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anapanganso zipangizo za gomelo, mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo, za golide woona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anapanga ziwiya za pa tebulolo zagolide wabwino, mbale ndi zipande, mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe za chakumwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anapanganso zipangizo za gomelo, mbale zace, ndi zipande zace, ndi mitsuko yace, ndi zikho zace zakuthira nazo, za golidi woona.