Exodus 37:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adapanga choikaponyale cha golide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi thunthu lake zinali zagolide, ndipo zonse zinali zosula ndi nyundo. Zikho zake, ndiye kuti nkhunje ndi maluŵa ake, adazipangira kumodzi ndi choikaponyalecho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga choikapo nyali cha golide woona; mapangidwe ake a choikapo nyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m'mwemo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anapanga choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zinasulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zinapangidwa kumodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga coikapo nyali ca golidi woona; mapangidwe ace a coikapo nyalico anacita cosula, tsinde lace ndi thupi lace, zikho zace, mitu yace, ndi maluwa ace zinakhala zocokera m'mwemo;