Exodus 37:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Guwa lofukizirapo lubani adalipanga ndi matabwa a mtengo wa kasiya. Linali lalibanda, muutalika mwake munali masentimita 46, muufupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 91, ndipo nyanga zake zidapangidwira kumodzi ndi guwalo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wakasiya; utali wake mkono, ndi kupingasa kwake mkono, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zinatuluka m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anapanga guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. Linali lofanana mbali zonse, mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91, ndipo nyanga zake zinapangidwa kumodzi ndi guwalo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wasitimu; utali wace mkono, ndi kupingasa kwace mkono, lampwamphwa; ndimsinkhu wace mikono iwiri; nyanga zace zinaturuka m'mwemo.