Exodus 38:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adapanga guwa la nsembe zopsereza la matabwa a mtengo wa kasiya. Linali lalibanda, muutali mwake munali masentimita 229, muufupi mwakenso ngati masentimita 229 mbali zonse zinali zofanana, msinkhu wake ngati masentimita 137.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wakasiya; utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono itatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa amtengo wa mkesha. Linali lofanana mbali zonse. Msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi masentimita 229.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wasitimu; utali wace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, lampwamphwa; ndi msinkhu wace mikono itaru.