Exodus 38:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku mbali yakumpoto kunali nsalu zochingira, kutalika kwake mamita 46. Nsanamira zake makumi aŵiri ndi masinde makumi aŵiri zinali zamkuŵa. Koma ngoŵe za pa nsanamirazo, pamodzi ndi mitanda yake, zinali zasiliva.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ake makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbali yakumpoto inalinso yotalika mamita 46 ndipo inali ndi mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsici zace makumi awiri, nw makamwa ace makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace yasiliva.