Exodus 38:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali nsalu zochinga pa mbali imodzi ya chipata, zotalika mamita asanu ndi aŵiri, zokhala ndi nsanamira zake zitatu ndi masinde atatu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nsalu zochingira za pa mbali imodzi ya chipata nza mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbali imodzi yachipata kunali nsalu yotchinga yotalika mamita asanu ndi awiri, mizati itatu ndi matsinde atatu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nsaru zocingira za pa mbali imodzi ya cipata nza mikono khumi ndi isanu; nsici zace zitatu, ndi makamwa ace atatu;