Exodus 38:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masinde a nsanamirazo anali opangidwa ndi mkuŵa. Ndipo ngoŵe za pa nsanamirazo, mitanda yake ndi zokutira nsonga za nsanamirazo, zonsezo zinali zasiliva. Nsanamira zonse za bwalolo zidalumikizidwa ndi mitanda yasiliva.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo makamwa a nsichi anali amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva; ndi zokutira mitu yake zasiliva; ndi nsichi zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Matsinde amizati anali amkuwa. Ngowe ndi zingwe za mizati zinali zasiliva, ndipo pamwamba pa mizatiyo anakutapo siliva. Choncho mizati yonse ya bwalolo inalumikizidwa ndi zingwe zasiliva.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo makamwa a nsici anali amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda Iyace zasiliva; ndi zokutira mitu yace zasiliva; ndi nsici zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.