Exodus 38:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nsalu zochingira pa chipata cha ku bwalolo, zokongoletsedwa ndi zopetapeta, zinali zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, ndiponso za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Kutalika kwake kunali mamita asanu ndi anai, msinkhu wake unali masentimita 229 monga zochingira zake za bwalolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo ndiyo ntchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake ndi kupingasa kwake mikono isanu, yolingana ndi nsalu zochingira za pabwalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nsalu yotchinga ya pa chipata inali yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira, yofewa yosalala ndi yopangidwa ndi anthu aluso. Nsaluyo inali yotalika mamita asanu ndi anayi, molingana ndi nsalu zotchinga bwalo. Msinkhu wake unali masentimita 229,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo ndiyo nchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mu kupingasa kwace mikono isanu, yolingana ndi nsaru zocingira za pabwalo.