Exodus 38:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nachi chiŵerengero cha golide, siliva ndi mkuŵa zimene ankazigwiritsa ntchito m'chihema chaumboni cha Chauta, monga momwe Mose adalamulira. Alevi ndiwo anali ndi udindo wakuziŵerenga, ndipo amene ankaŵatsogolera ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ichi ndi chiwerengo cha zinthu za chihema, chihema cha mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, achite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chiwerengero cha zipangizo zimene anagwiritsa ntchito popanga chihema, chihema chaumboni, zimene Mose analamulira Alevi kuti alembe motsogozedwa ndi Itamara mwana wa Aaroni, wansembe, chinali ichi:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ici ndi ciwerengo ca zinthu za cihema, cihema ca mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, acite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.